1 Chronicles 1:43 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Naŵa mafumu amene ankalamulira ku dziko la Edomu, Aisraele adakalibe mfumu iliyonse: Bela mwana wa Beori, ndipo mzinda wake unali Dinaba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mafumu tsono akuchita ufumu m'dziko la Edomu, pakalibe mfumu wakuchita ufumu pa ana a Israele, ndiwo Bela mwana wa Beori; ndi dzina la mudzi wake ndilo Dinihaba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Awa ndi mafumu amene ankalamulira dziko la Edomu, mfumu iliyonse ya Israeli isanayambe kulamulira kumeneko: Bela mwana wa Beori, mzinda wake ankawutcha Dinihaba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mafumu tsono akucita ufumu m'dziko la Edomu, pakalibe mfumu wakucita ufumu pa ana a Israyeli, ndiwo Bela mwana wa Beori; ndi dzina la mudzi wace ndilo Dinaba.