1 Chronicles 1:44 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Bela atafa, Yobabu mwana wa Zera wa ku Bozira, adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anafa Bela; ndi Yobabu mwana wa Zera wa ku Bozira anakhala mfumu m'malo mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Bela atamwalira, Yobabu mwana wa Zera wochokera ku Bozira analowa ufumu mʼmalo mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anafa Bela; ndi Yobabi mwana wa Zera wa ku Bozra anakhala mfumu m'malo mwace.