1 Chronicles 1:50 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Baala-Hanani atafa, Hadadi adaloŵa ufumu m'malo mwake. Mzinda wake ankautchula kuti Pai. Mkazi wake anali Metabele mwana wa Materedi, mwana wa Mezahabu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Namwalira Baala-Hanani; ndi Hadadi anakhala mfumu m'malo mwake; ndipo dzina la mudzi wake ndi Pai; ndi dzina la mkazi wake ndiye Mehetabele mwana wamkazi wa Matiredi mwana wamkazi wa Mezahabu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Baala-Hanani anamwalira, Hadadi analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Pau, ndipo dzina la mkazi wake linali Mehatabeli mwana wa Matiredi, mwana wamkazi wa Me-Zahabu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Namwalira Baalahanani; ndi Hadada anakhala mfumu m'malo mwace; ndipo dzina la mudzi wace ndi Pai; ndi dzina la mkazi wace ndiye Mehetabele mwana wamkazi wa Matradi mwana wamkazi wa Mezahabu.