1 Chronicles 10:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Saulo adafa chifukwa cha kusakhulupirika kwake. Iyeyo anali wosakhulupirika kwa Chauta, poti sankamvera mau a Chauta ndiponso ankapempha nzeru kwa anthu olankhula ndi mizimu,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo Saulo anafa, chifukwa cha kulakwa kwake analakwira Yehova, kulakwira mau a Yehova amene sanawasunge; ndiponso chifukwa cha kufunsira wobwebweta, kufunsirako,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sauli anafa chifukwa anali wosakhulupirika pamaso pa Yehova. Iye sanasunge mawu a Yehova, pakuti anakafunsira nzeru kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo Sauli anafa, cifukwa ca kulakwa kwace analakwira Yehova, kulakwira mau a Yehova amene sanawasunga; ndiponso cifukwa ca kufunsira wobwebweta, kufunsirako,