1 Chronicles 10:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Saulo adauza wonyamula zida zake kuti, “Solola lupanga lako, undibaye, kuwopa kuti anthu osaumbalidwaŵa akabwera angadzandiseke.” Koma wonyamula zida uja sadathe kuchita zimenezo, chifukwa ankachita mantha kwambiri. Ndiye Saulo adangotenga lupanga lake nagwerapo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Saulo anati kwa wonyamula zida zake, Solola lupanga lako, nundipyoze nalo, angafike osadulidwa awa ndi kundiseka. Koma wonyamula zida zake anakana, popeza anaopa kwambiri. Pomwepo Saulo anatenga lupanga lake, naligwera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Sauli anawuza mnyamata wake wonyamula zida zake kuti, “Solola lupanga lako undiphe, kuopa kuti anthu osachita mdulidwewa angabwere ndi kudzandizunza ine.” Koma mnyamata wonyamula zida uja anachita mantha kwambiri ndipo sanathe kutero. Choncho Sauli anatenga lupanga lake lomwe nagwerapo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Sauli anati kwa wonyamula zida zace, Solola lupanga lako, nundipyoze nalo, angafike osadulidwa awa ndi kundiseka, Koma wonyamula zida zace anakana, popeza anaopa kwambiri. Pomwepo Sauli anatenga lupanga lace, naligwera.