1 Chronicles 10:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele onse amene anali ku chigwa, ataona kuti gulu lankhondo lathaŵa, ndipo kuti Saulo ndi ana ake aphedwa, nawonso adathaŵa nasiya mizinda yao. Tsono Afilisti aja adabwera nkudzakhala m'menemo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene amuna onse a Israele okhala m'chigwamo anaona kuti anathawa, ndi kuti Saulo ndi ana ake adafa, anasiya midzi yao, nathawa; nadza Afilisti, nakhala m'menemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Aisraeli onse amene anali mʼchigwa anaona kuti gulu lankhondo lathawa komanso kuti Sauli ndi ana ake aphedwa, nawonso anathawa kusiya mizinda yawo. Ndipo Afilisti anabwera kudzakhalamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene amuna onse a Israyeli okhala m'cigwamo anaona kuti anathawa, ndi kuti Sauli ndi ana ace adafa, anasiya midzi yao, nathawa; nadza Afilisti, nakhala m'menemo.