1 Chronicles 10:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adamdula mutu Sauloyo, namuvula zida zake zankhondo. Kenaka adatuma amithenga ku dziko lao lonse, kuti akafalitse uthenga wabwinowu kwa milungu yao ndi kwa anthu omwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamvula natenga mutu wake, ndi zida zake, natumiza ku dziko la Afilisti pozungulirapo, kulalika m'mafano ao ndi mwa anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anamuvula zovala zake, natenga mutu wake ndi zida zake zankhondo. Ndipo anatumiza amithenga mʼdziko lonse la Afilisti kukafalitsa nkhani yabwinoyi kwa mafano awo ndi kwa anthu awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anambvula natenga mutu wace, ndi zida zace, natumiza ku dziko la Afilisti pozungulirapo, kulalika m'mafano ao ndi mwa anthu.