1 Chronicles 11:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono aŵa ndiwo atsogoleri a nkhondo a Davide, amene ankamthandiza pamodzi ndi Aisraele onse, kuti akhale mfumu potsata mau a Chauta onena za Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akulu a amphamvu aja Davide anali nao akulimbika pamodzi naye m'ufumu wake, pamodzi ndi Aisraele onse, kumlonga ufumu, monga mwa mau a Yehova akunena za Israele, ndi awa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Awa ndiye anali atsogoleri amphamvu a Davide. Iwo pamodzi ndi Aisraeli onse, anathandiza kulimbikitsa ufumu wake kuti ukwanire madera onse, monga momwe Yehova analonjezera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akuru a amphamvu aja Davide anali nao akulimbika pamodzi naye m'ufumu wace, pamodzi ndi Aisrayeli onse, kumlonga ufumu, monga mwa mau a Yehova akunena za Israyeli, ndi awa.