1 Chronicles 11:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyo anali pamodzi ndi Davide ku Pasidamimu pamene Afilisti adaasonkhana kumeneko kuti amenyane naye nkhondo. Kumeneko kudaali munda wodzaza ndi barele ndipo anthu a Davide adathaŵa kuwopa Afilistiwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anali pamodzi ndi Davide ku Pasidamimu muja; Afilisti anasonkhanako kunkhondo kumene kunali munda wodzala ndi barele; ndipo anthu anathawa pamaso pa Afilisti.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anali ndi Davide ku Pasi-Damimu pamene Afilisti anasonkhana kudzachita nkhondo. Ankhondo anathawa Afilistiwo pamalo pamene panali munda wodzaza ndi barele.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anali pamodzi ndi Da vide ku Pasidamimu muja; Afilisti anasonkhanako kunkhondo kumene kunali munda wodzala ndi barele; ndipo anthu anathawa pamaso pa Afilisti.