1 Chronicles 11:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Eleazara ndi anzake adakaima m'kati mwa mundawo nautchinjiriza, ndipo adapha Afilistiwo. Motero Chauta adaŵapulumutsa ndi kuŵapambanitsa kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma anadziimika pakati pa munda, naulanditsa, nakantha Afilisti; m'mwemo anawapulumutsa Yehova ndi chipulumutso chachikulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma awiriwo anayima pakati pa mundawo. Iwo anawuteteza, nakantha Afilistiwo ndipo Yehova anawapambanitsa koposa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma anadziimika pakati pa munda, naulanditsa, nakantha Afilisti; m'mwemo anawapulumutsa Yehova ndi cipulumutso cacikuru.