1 Chronicles 11:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye Davide atamva ludzu kwambiri adati, “Ha, wina akadandipatsa madzi a m'chitsime chimene chili pafupi ndi chipata ku Betelehemu kuti ndimwe!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide analakalaka, nati, Ha? Mwenzi wina atandimwetsa madzi a m'chitsime cha ku Betelehemu chili kuchipata.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide analakalaka madzi ndipo anati, “Haa, pakanapezeka munthu wokanditungira madzi a mʼchitsime chomwe chili pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide analakalaka, nati, Ha! mwenzi wina atandimwetsa madzi a m'citsime ca ku Betelehemu ciri kucipata,