1 Chronicles 11:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pomwepo anthu atatu amphamvu aja adapita akubzola zithando za Afilisti, nakatunga madzi ku chitsime cha ku Betelehemu, chimene chinali pafupi ndi chipata. Adatenga madziwo nabwera nawo kwa Davide. Koma Davideyo sadafune kumwako madziwo, adangoŵathira pansi kuŵapereka kwa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Napyola atatuwo misasa ya Afilisti natunga madzi ku chitsime cha ku Betelehemu chili kuchipata, nabwera nao kwa Davide; koma Davide anakana kumwako, koma anawathirira kwa Yehova;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho anthu atatuwa anadutsa mizere ya Afilisti, natunga madzi amene anali mʼchitsime chomwe chinali pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu nabwera nawo kwa Davide. Koma iye anakana kumwa. Mʼmalo mwake anathira pansi pamaso pa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Napyola atatuwo misasa ya Afilish natunga madzi ku citsime ca ku Betelehemu ciri kucipata, nabwera nao kwa Davide; koma Davide anakana kumwako, koma anawathirira kwa Yehova;