1 Chronicles 11:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo adati, “Ndithu, pali Mulungu, sindingachite chinthu chotere, chifukwa kukhala ngati kumwa magazi a anthuŵa amene adaika moyo wao pa minga, pang'ono akadataya moyo wao pokabwera nawo madzi ameneŵa.” Motero adakana kumwa madziwo. Zimenezi ndizo adachita anthu atatu amphamvu aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nati, Pali Mulungu wanga, kukhale kutali kwa ine kuchita ichi. Ngati ndidzamwa mwazi wa anthu awa? Akadataya moyo wao, inde akadataya moyo wao, pakukatenga madziwa. M'mwemo sanafune kuwamwa. Izi anazichita atatu amphamvuwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anati, “Inu Mulungu, musalole kuti ine ndichite chinthu ichi! Kodi ndimwe magazi a anthu amene anayika miyoyo yawo pachiswe?” Chifukwa iwo anayika miyoyo yawo pachiswe kuti abweretse madziwo, Davide sanamwe. Zimenezi ndi zimene anachita anthu amphamvu atatuwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nati, Pali Mulungu wanga, kukhale kutali kwa ine kucita ici. Ngati ndidzamwa mwazi wa anthu awa? Akadataya moyo wao, inde akadataya moyo wao, pakukatenga madziwa. M'mwemo sanafuna kuwamwa. Izi anazicita atatu amphamvuwa.