1 Chronicles 11:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kale, ngakhale Saulo adakali mfumu yathu yotilamulira, ndinuyo amene munkatsogolera Aisraele ku nkhondo, nkumabwera nawonso. Ndipo Chauta, Mulungu wanu, adaakuuzani kuti, ‘Udzakhala mbusa wa anthu anga Aisraele, udzakhala mfumu ya anthu anga Aisraele.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngakhale kale lomwe, pokhala mfumu Sauloyo, wotuluka ndi kulowa nao Aisraele ndinu; ndipo Yehova Mulungu wanu anati kwa inu, Uzidyetsa anthu anga Aisraele, nukhale mtsogoleri wa anthu anga Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kale lija, ngakhale pamene Sauli anali mfumu, inu ndinu amene munkatsogolera Aisraeli pa nkhondo zawo. Ndipo Yehova Mulungu wanu anakuwuzani kuti, ‘Iwe udzaweta anthu anga Aisraeli, ndipo udzakhala mfumu yawo.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngakhale kale lomwe, pokhala mfumu Sauliyo, woturuka ndi kulowa nao Aisrayeli ndinu; ndipo Yehova Mulungu wanu anati kwa inu, Uzidyetsa anthu anga Aisrayeli, nukhale mtsogoleri wa anthu anga Israyeli.