1 Chronicles 11:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abisai, mbale wake wa Yowabu, anali mkulu wa atsogoleri makumi atatu aja. Ndiye adapha ndi mkondo wake anthu 300, nakhala wotchuka ngati anthu atatu aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abisai mbale wa Yowabu, ndiye wamkulu wa atatuwa; pakuti anasamulira mazana atatu mkondo wake, nawapha, namveka dzina pakati pa atatuwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abisai mʼbale wa Yowabu ndiye anali mtsogoleri wa anthu atatuwa. Iye anapha ndi mkondo ankhondo 300. Choncho iyeyo anali wotchuka pakati pa anthu atatu aja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abisai mbale wa Yoabu, ndiye wamkuru wa atatuwa; pakuti anasamulira mazana atatu mkondo wace, nawapha, namveka dzina pakati pa atatuwa.