1 Chronicles 11:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye anali womveka kwambiri mwa atsogoleri makumi atatu aja, ndipo adasanduka mkulu wao, komabe sadafikepo pa anthu atatu aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwa atatuwa iye anali waulemu woposa awiriwa, nasanduka mkulu wao; koma sanafike pa atatu oyamba aja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye analandira ulemu woposa atatuwo. Kotero anakhala mtsogoleri wawo ngakhale kuti iyeyo sanali mʼgulu la anthu atatu aja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwa atatuwa iye anali waulemu woposa awiriwa, nasanduka mkuru wao; koma sanafikana nao atatu oyamba aja.