1 Chronicles 11:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Benaya mwana wa Yehoyada wa ku Kabizeele, anali munthu wolimba mtima, amene ankachita ntchito zazikulu. Iyeyo adapha ngwazi ziŵiri za ku Mowabu. Tsiku lina chisanu cha mbee chitagwa adatsikira m'chitsime, naphamo mkango.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Benaya mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi ya ku Kabizeeli, wochita zachikulu, anapha ana awiri a Ariyele wa ku Mowabu; anatsikanso, napha mkango m'kati mwa dzenje nyengo ya chipale chofewa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Benaya mwana wa Yehoyada wa ku Kabizeeli anali munthu wolimba mtima amene anachita zinthu zamphamvu. Iye anakantha ankhondo awiri otchuka a ku Mowabu. Tsiku lina kukuzizira kwambiri, iye analowa mʼdzenje ndi kuphamo mkango.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Benaya mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi ya ku Kabzeeli, wocita zazikuru, anapha ana awiri a Ariyeli wa ku Moabu; anatsikanso, napha mkango m'kati mwa dzenje nyengo ya cipale cofewa.