1 Chronicles 11:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaphanso Mwejipito wina wamkulu thupi, kutalika kwake ngati mamita aŵiri ndi theka. Mwejipitoyo anali ndi mkondo m'manja wofanafana ndi mtanda wa munthu woomba nsalu. Koma Benaya adapita kwa iyeyo atatenga ndodo, nalanda mkondowo kumanja kwa Mwejipito uja, nkumupha ndi mkondo wake womwewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anaphanso Mwejipito munthu wamkulu, msinkhu wake mikono isanu, ndi m'dzanja la Mwejipito munali mkondo ngati mtanda woombera nsalu; ndipo anamtsikira ndi ndodo, nakwatula mkondo m'dzanja la Mwejipito, namupha ndi mkondo wake womwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo iye anakanthanso Mwigupto amene anali wotalika mamita awiri ndi theka. Ngakhale kuti Mwiguptoyo anali ndi mkondo wofanana ndi ndodo yowombera nsalu mʼdzanja mwake, Benaya anapita kukamenyana naye ali ndi chibonga chokha mʼmanja. Iye analanda mkondo mʼdzanja la Mwiguptoyo ndi kumupha ndi mkondo wake womwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anaphanso M-aigupto munthu wamkuru, msinkhu wace mikono isanu, ndi m'dzanja la M-aigupto munali mkondo ngati mtanda woombera nsaru; ndipo anamtsikira ndi ndodo, nakwatula mkondo m'dzanja la M-aigupto, namupha ndi mkondo wace womwe.