1 Chronicles 11:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimenezi ndizo adachita Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo adatchuka ngati atsogoleri makumi atatu amphamvu aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Izi anazichita Benaya mwana wa Yehoyada, namveka dzina mwa atatu amphamvuwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Izi ndi zamphamvu zimene Benaya mwana wa Yehoyada anachita. Iyeyo analinso wotchuka ngati anthu atatu amphamvu aja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Izi anazicita Benaya mwana wa Yehoyada, namveka dzina mwa atatu amphamvuwo.