1 Chronicles 11:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyu anali womveka mwa atsogoleri makumi atatuwo, komabe sadafikepo pa anthu atatu aja. Davide adamuika kuti azilamulira asilikali ake omuteteza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, anali wa ulemu woposa makumi atatuwo, koma sanafike pa atatu oyamba aja; ndipo Davide anamuika mkulu wa olindirira ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye ankalemekezedwa kuposa wina aliyense mwa anthu makumi atatu, koma sanali mʼgulu la anthu atatu aja. Ndipo Davide anamuyika kukhala woyangʼanira asilikali omuteteza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, anali wa ulemu woposa makumi atatuwo, koma sanafikana atatu oyamba aja; ndipo Davide anamuika mkuru wa olindirira ace.