1 Chronicles 11:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho atsogoleri onse a Aisraele adadza kwa mfumu ku Hebroni. Tsono Davide adachita nawo chipangano pamaso pa Chauta ku Hebroniko, ndipo anthuwo adamdzoza Davideyo kuti akhale mfumu ya Aisraele onse, potsata mau a Chauta ochokera m'kamwa mwa Samuele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akulu onse omwe a Israele anadza kwa mfumu ku Hebroni; ndipo Davide anapangana nao pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova; ndipo anamdzoza Davide akhale mfumu ya Israele monga mwa mau a Yehova, ndi dzanja la Samuele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akuluakulu onse a Israeli atafika kwa Mfumu Davide ku Hebroni, iye anachita nawo pangano pamaso pa Yehova, ndipo anamudzoza Davide kukhala mfumu ya Israeli, monga momwe Yehova analonjezera kudzera mwa Samueli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akuru onse omwe a Israyeli anadza kwa mfumu ku Hebroni; ndipo Davide anapangana nao pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova; ndipo anamdzoza Davide akhale mfumu ya Israyeli monga mwa mau a Yehova, ndi lizanja la Samueli.