1 Chronicles 11:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide anali atanena kuti, “Aliyense amene ayambe kukantha Ayebusi, adzakhala mkulu wolamulira gulu lankhondo.” Tsono Yowabu mwana wa Zeruya ndiye adayamba kupitako, motero adakhala mtsogoleri wankhondo woyamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati Davide, Aliyense woyamba kukantha Ayebusi, yemweyo adzakhala mkulu ndi mtsogoleri. Nayamba kukwerako Yowabu mwana wa Zeruya, nakhala mkulu iyeyu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anali atanena kuti “Aliyense amene adzatsogolere kukathira nkhondo Ayebusi adzakhala mkulu wa asilikali.” Yowabu mwana wa Zeruya ndiye anayamba kupita, motero anakhala mkulu wa asilikali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati Davide, Ali yense woyamba kukantha Ayebusi, yemweyo adzakhala mkulu ndi mtsogoleri. Nayamba kukwerako Yoabu mwana wa Zeruya, nakhala mkuru iyeyu.