1 Chronicles 12:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Naŵa anthu amene adadza kwa Davide ku Zikilagi, kumene Davideyo adaathaŵira chifukwa choopa Saulo mwana wa Kisi. Anthu ameneŵa ankathandiza Davide kumenya nkhondo, pamodzi ndi anzao amphamvu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anadzawo kwa Davide ku Zikilagi, akali chitsekedwere chifukwa cha Saulo mwana wa Kisi, ndi awa; ndiwo mwa amphamvuwo omthandiza kunkhondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nawa anthu amene anabwera kwa Davide ali ku Zikilagi pamene iye anathamangitsidwa ndi Sauli mwana wa Kisi (iwowo anali mʼgulu la asilikali amene ankamuthandiza pa nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anadzawo kwa Davide ku Zikilaga, akali citsekedwere cifukwa ca Sauli mwana wa Kisi, ndi awa; ndiwo mwa amphamvuwo omthandiza kunkhondo.