1 Chronicles 12:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Agadi ameneŵa ndiwo amene anali m'gulu la atsogoleri ankhondo. Ang'onoang'ono ankalamulira anthu 100, pamene akuluakulu ankalamulira anthu 1,000.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Awa a ana a Gadi, anali atsogoleri a nkhondo; wamng'ono wa iwo anayang'anira zana limodzi, ndi wamkulu wa iwo anayang'anira chikwi chimodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a fuko la Gadi amenewa anali atsogoleri; angʼonoangʼono amalamulira anthu 100 pamene akuluakulu amalamulira anthu 1,000.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Awa a ana a Gadi, anali atsogoleri a nkhondo; wamng'ono wa iwo anayang'anira zana limodzi, ndi wamkuru wa iwo anayang'anira cikwi cimodzi.