1 Chronicles 12:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ameneŵa ndiwo anthu amene adaoloka Yordani mwezi woyamba, nthaŵi imene mtsinjewo unali wodzaza nkumasefukira pa zibumi zake zonse. Motero adapirikitsa anthu onse amene anali m'zigwa. Ena kuthaŵira kuvuma ena kuzambwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Awa ndi omwe aja anaoloka Yordani mwezi woyamba, atadzala kusefukira magombe ake onse; nathawitsa onse okhala m'zigwa kum'mawa ndi kumadzulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Awa ndi amene anawoloka Yorodani mwezi woyamba pamene mtsinje unali utasefukira mbali zonse, ndipo anathamangitsa aliyense amene amakhala mʼchigwa, mbali ya kumadzulo ndi kummawa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Awa ndi omwe aja anaoloka Yordano mwezi woyamba, atadzala kusefukira magombe ace onse; nathawitsa onse okhala m'zigwa kum'mawa ndi kumadzulo.