1 Chronicles 12:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide adatuluka kukakumana nawo, ndipo adaŵauza kuti, “Ngati mwadza kwa ine kuno mwaubwenzi kuti mudzandithandize, ndiye kuti mtima wanga udzagwirizana nanu. Koma ngati nkundipereka kwa adani anga, ngakhale sindidalakwe, pamenepo Mulungu wa makolo athu apenye ndipo akulangeni.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anatuluka kukomana nao, nayankha, nanena nao, Ngati mwandidzera mwamtendere kundithandiza, mtima wanga udzalumikizana nanu; koma ngati mwafika kundipereka kwa adani anga, popeza m'manja mwanga mulibe chiwawa, Mulungu wa makolo athu achione ndi kuchilanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anapita kukakumana nawo ndipo anati, “Ngati mwabwera kwa ine mwamtendere, kuti mundithandize, ndakonzeka kugwirizana nanu. Koma ngati mwabwera kudzandipereka kwa adani anga, ngakhale kuti sindinalakwe, Mulungu wa makolo anthu aone izi ndipo akuweruzeni.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anaturuka kukomana nao, nayankha, nanena nao, Ngati mwandidzera mwamtendere kundithandiza, mtima wanga udzalumikizana nanu; koma ngati mwafika kundipereka kwa adani anga, popeza m'manja mwanga mulibe ciwawa, Mulungu wa makolo athu acione ndi kucilanga.