1 Chronicles 12:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pomwepo Mzimu wa Mulungu udamtsikira Amasai, mtsogoleri wa anthu makumi atatu aja, ndipo adati, “Inu Davide, ifetu ndife anu. Tili limodzi nanu, inu mwana wa Yese. Inu ndi anthu amene amakuthandizani, mudzakhala opambana. Zoonadi Mulungu wanu ali nanu.” Tsono Davide adaŵalandira ndipo adaŵasandutsa atsogoleri a magulu ake ankhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mzimu unavala Amasai, ndiye wamkulu wa makumi atatuwo, nati iye, Ndife anu, Davide, tivomerezana nanu mwana wa Yese inu: mtendere, mtendere ukhale ndi inu, ndi mtendere ukhale ndi athandizi anu; pakuti Mulungu wanu akuthandizani. Ndipo Davide anawalandira, nawaika akulu a magulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Mzimu anabwera pa Amasai, mtsogoleri wa anthu makumi atatu aja ndipo anati: “Inu Davide, ife ndife anu! Tili nanu limodzi, inu mwana wa Yese! Kupambana, Kupambana kwa inu, ndiponso kupambana kukhale kwa iwo amene akukuthandizani pakuti Mulungu wanu adzakuthandizani.” Kotero Davide anawalandira ndipo anawayika kukhala atsogoleri a magulu ake a ankhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mzimu unabvala Amasai, ndiye wamkuru wa makumi atatuwo, nati iye, Ndife anu, Davide, tibvomerezana nanu mwana wa Jese inu: mtendere, mtendere ukhale ndi inu, ndi mtendere ukhale ndi athandizi anu; pakuti Mulungu wanu akuthandizani. Ndipo Davide anawalandira, nawaika akuru a magulu.