1 Chronicles 12:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ena a fuko la Manase adabwera kwa Davide nthaŵi imene Davide adadza ndi Afilisti kudzamenyana nkhondo ndi Saulo. Komabe nthaŵiyo Davide sadaŵathandize Afilisti, poti akazembe ao adambweza namanena kuti, “Uyu akhoza kubwerera kwa mbuye wake Saulo, ndiye ife tidzaonongeka pamenepo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ena a Manase omwe anapatukira kwa Davide, muja iye anadza ndi Afilisti koponyana nkhondo ndi Saulo, koma sanawathandiza; popeza akalonga a Afilisti, atachita upo, anamuuza achoke, ndi kuti, Adzapatukira kwa mbuye wake Saulo ndi kutisandulikira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu ena a fuko la Manase anathawira kwa Davide pamene anapita ndi Afilisti kukamenyana ndi Sauli. (Iye ndi anthu ake sanathandize Afilisti chifukwa, atsogoleri awo atakambirana, anamubweza Davide. Iwo anati, “Ife tidzawonongedwa ngati uyu adzabwerera kwa mbuye wake Sauli).”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ena a Manase omwe anapambukira kwa Davide, muja iye anadza ndi Afilisti koponyana nkhondo ndi Sauli, koma sanawathandiza; popeza akalonga a Afilisti, atacita upo, anamuuza acoke, ndi kuti, Adzapambukira kwa mbuye wace Sauli ndi kutisandulikira.