1 Chronicles 12:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero pamene Davide ankabwerera ku Zikilagi, anthu a fuko la Manase aja adapita naye limodzi. Amanasewo anali aŵa: Adina, Yozabadi, Yediyaele, Mikaele, Yozabadi, Elihu ndi Ziletai, atsogoleri a magulu a ankhondo zikwi zambiri a ku Manase.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomuka iye ku Zikilagi anapatukira kwa iye a Manase: Adina, ndi Yozabadi, ndi Yediyaele, ndi Mikaele, ndi Yozabadi, ndi Elihu, ndi Ziletai, akulu a zikwi a ku Manase.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide atapita ku Zikilagi, anthu a fuko la Manase amene anathawira kwa iye anali awa: Adina, Yozabadi, Yediaeli, Mikayeli, Yozabadi, Elihu ndi Ziletai; atsogoleri a magulu a anthu 1,000 a ku Manase.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomuka iye ku Zikilaga anapambukira kwa iye a Manase: Adina, ndi Yozabadi, ndi Yedyaeli, ndi Mikaeli, ndi Yozabadi, ndi Elihu, ndi Ziletai, akuru a zikwi a ku Manase.