1 Chronicles 12:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nachi chiwerengero cha magulu a anthu ankhondo amene adadza ku Hebroni kwa Davide, kudzamlonga ufumu m'malo mwa Saulo, potsata mau a Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kuwerenga kwa akulu okonzekeratu kunkhondo, anadzawo kwa Davide ku Hebroni, kupambukitsa ufumu wa Saulo ukhale wake, monga mwa mau a Yehova, ndi uku.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nachi chiwerengero cha magulu a anthu ankhondo amene anabwera kwa Davide ku Hebroni kudzapereka ufumu wa Sauli kwa iye, monga momwe ananenera Yehova:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kuwerenga kwa akuru okonzekeratu kunkhondo, anadzawo kwa Davide ku Hebroni, kupambukitsa ufumu wa Sauli ukhale wace, monga mwa mau a Yehova, ndi: uku.