1 Chronicles 12:38 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ankhondo onseŵa amene ankadziŵa kamenyedwe ka nkhondo, adadza ku Hebroni ndi mtima umodzi, kuti akamlonge ufumu Davide. Aisraele onse nawonso anali ndi mtima womwewo wofuna kumlonga ufumu Davide.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Onsewa, ndiwo anthu a nkhondo akusunga malongosoledwe a nkhondo, anadza ku Hebroni ndi mtima wangwiro kudzamlonga Davide mfumu ya Aisraele onse; ndi onse otsala a Israele omwe anali a mtima umodzi kumlonga Davide ufumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onsewa anali anthu odziwa kumenya nkhondo amene anadzipereka ku magulu awo. Iwo anabwera ku Hebroni ali otsimikiza kudzamuyika Davide kukhala mfumu ya Aisraeli. Aisraeli ena onse anali ndi mtima umodzinso womuyika Davide kukhala mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Onsewa, ndiwo anthu a nkhondo akusunga malongosoledwe a nkhondo, anadza ku Hebroni ndi mtima wangwiro kudzamlonga Davide mfumu ya Aisraeli onse; ndi onse otsala a Israyeli omwe anali a mtima umodzi kumlonga Davide ufumu.