1 Chronicles 12:40 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nawonso anansi ao, ochokera ngakhale ku Isakara ndi Zebuloni ndi Nafutali, adadza atasenzetsa chakudya abulu ao, ngamira zao, nyulu zao ndi ng'ombe zao. Adazisenzetsa chakudya chambiri, makeke ankhuyu, ntchichi zamphesa, vinyo ndiponso mafuta. Adabweranso ndi ng'ombe ndi nkhosa zambiri, poti ku dziko la Israele kunali chisangalalo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso akuyandikizana nao mpaka Isakara ndi Zebuloni ndi Nafutali anabwera nao mkate osenzetsa abulu, ndi ngamira, ndi nyuru, ndi ng'ombe, zakudya zaufa, ndi nchinchi zankhuyu, ndi nchinchi zamphesa, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi ng'ombe, ndi nkhosa zochuluka; pakuti munali chimwemwe m'Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komanso anthu oyandikana nawo ochokera ku Isakara, Zebuloni ndi Nafutali anabweretsa zakudya pa abulu, ngamira, nyulu ndi ngʼombe. Panali ufa wambiri, makeke ankhuyu, ntchintchi za mphesa, vinyo, mafuta, ngʼombe, nkhosa ndi mbuzi, popeza munali chimwemwe mu Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso akuyandikizana nao mpaka Isakara ndi Zebuloni ndi Nafitali anabwera nao mkate osenzetsa aburu, ndi ngamira, ndi nyuru, ndi ng'ombe, zakudya zaufa, ndi ncinci zankhuyu, ndi ncinci zamphesa, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi ng'ombe, ndi nkhosa zocuruka; pakuti munali cimwemwe m'Israyeli.