1 Chronicles 12:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Asilikali ena amphamvu, ochokera ku dziko la Gadi, adafika kwa Davide ku linga lake lam'chipululu. Iwoŵa anali ngwazi zodziŵa kumenya nkhondo, makamaka pogwiritsa ntchito chishango ndi mkondo, ndipo anali oopsa ngati mikango. Akamathamanga, ngati ngoma zam'mapiri liŵiro lake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi Agadi ena anapatukira kwa Davide ku linga la m'chipululu, ngwazi zamphamvu zozerewera nkhondo, zogwira chikopa ndi mkondo; nkhope zao zikunga nkhope za mikango, ndi liwiro lao longa la ngoma mumapiri:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Asilikali ena a fuko la Gadi anathawira kwa Davide ku linga lake ku chipululu. Iwo anali asilikali olimba mtima, okonzekera nkhondo ndipo amadziwa kugwiritsa ntchito chishango ndi mkondo. Iwowo anali woopsa ngati mikango ndipo anali aliwiro ngati ngoma zamʼmapiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi Agadi ena anapambukira kwa Davide ku liogala m'cipululu, ngwazi zamphamvu zozerewera nkhondo, zogwira cikopa ndi mkondo; nkhope zao zikunga nkhope za mikango, ndi liwiro lao longa la ngoma kumapiri: