1 Chronicles 13:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Davide adakhumudwa chifukwa chakuti Chauta adaakantha Uza. Ndipo mpaka pano malo amenewo amaŵatchula kuti Pereziuza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudaipira Davide kuti Yehova adachita chipasulo ndi Uza; motero anatcha malowo Pereziuza, mpaka lero lino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Davide anakhumudwa chifukwa Yehova anakantha Uza ndipo mpaka lero malowo amatchedwa Perezi Uza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudaipira Davide kuti Yehova adacita cipasulo ndi Uza; motero anacha malowo Perezi Uza, mpaka lero lino.