1 Chronicles 13:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake adauza msonkhano wonse wa Aisraele kuti, “Ngati zikukukomerani inu, ndipo ngati chimenecho ndiye chifuniro cha Chauta, Mulungu wathu, tiyeni titumize mau kwa abale athu onse amene akukhala m'dziko lonse la Israele ndiponso kwa ansembe ndi kwa Alevi okhala ku mizinda ndi ku miraga yake, kuti anthuwo adzasonkhane pamodzi kwa ife kuno.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anati kwa msonkhano wonse wa Israele, Chikakomera inu, ndipo chikachokera kwa Yehova Mulungu wathu, titumize konse kuti abale athu otsala m'dziko lonse la Israele, ndi ansembe ndi Alevi okhala nao m'midzi yao yokhala napo podyetsa, kuti asonkhane kwa ife;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anati kwa gulu lonse la Israeli, “Ngati kukukomerani komanso ngati chili chifuniro cha Yehova Mulungu wathu, tiyeni titumize uthenga kulikonse kumene kuli abale athu ena onse ku dziko lonse la Israeli ndiponso kwa ansembe ndi Alevi amene ali nawo mʼmidzi yawo ndi madera odyetsera ziweto, kuti abwere adzakhale nafe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anati kwa msonkhano wonse wa Israyeli, Cikakomera inu, ndipo cikacokera kwa Yehova Mulungu wathu, titumize konse kuti abale athu otsala m'dziko lonse la Israyeli, ndi ansembe ndi Alevi okhala nao m'midzi yao yokhala napa podyetsa, kuti asonkhane kwa ife;