1 Chronicles 13:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Davide pamodzi ndi Aisraele onse adakwera kupita ku Baala, ndiye kuti ku Kiriyati-Yearimu m'dera la ku Yuda, kuti akatenge Bokosi lachipangano la Mulungu. Bokosilo limadziŵika ndi dzina la Chauta amene amakhala pa akerubi ngati pa mpando waufumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide ndi Aisraele onse pamodzi naye anakwera kunka ku Baala, ndiko ku Kiriyati-Yearimu wa m'Yuda, kukwera nalo kuchokera komweko likasa la Mulungu Yehova wakukhala pa akerubi, kumene aitanirako Dzina.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide pamodzi ndi Aisraeli onse anapita ku Baalahi (Kiriati-Yearimu) ku Yuda kukatenga Bokosi la Yehova Mulungu, amene amakhala pakati pa akerubi. Limeneli ndiye Bokosi la Chipangano lomwe limadziwika ndi Dzina lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide ndi Aisrayeli onse pamodzi naye anakwera kumka ku Baala, ndiko ku Kiriati-Yearimu wa m'Yuda, kukwera nalo kucokera komweko likasa la Mulungu Yehova wakukhala pa akerubi, kumene aitanirako Dzina.