1 Chronicles 13:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Davide pamodzi ndi Aisraele onse anali ankakondwera kwambiri kulemekeza Mulungu poimba nyimbo ndi azeze, apangwe ndi ting'oma, ziwaya zamalipenga ndi malipenga amene.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide ndi Aisraele onse anasewera pamaso pa Mulungu ndi mphamvu yao yonse; ndi nyimbo, ndi azeze, ndi zisakasa, ndi malingaka, ndi nsanje, ndi malipenga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide pamodzi ndi Aisraeli onse ankakondwerera ndi mphamvu zawo zonse pamaso pa Mulungu, poyimba nyimbo pogwiritsa ntchito azeze, apangwe, matambolini, maseche ndi malipenga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide ndi Aisrayeli onse anasewera pamaso pa Mulungu ndi mphamvu yao yonse; ndi nyimbo, ndi azeze, ndi zisakasa, ndi malingaka, ndi nsanje, ndi malipenga,