1 Chronicles 14:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Hiramu, mfumu ya ku Tiro, adatuma amithenga kwa Davide, pamodzi ndi mitengo ya mkungudza ndiponso amisiri odziŵa kumanga ndi miyala ndi amisiri a matabwa, kuti akammangire nyumba Davideyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Huramu mfumu ya Tiro anatumiza mithenga kwa Davide, ndi mikungudza, ndi amisiri omanga miyala, ndi amatabwa, kuti ammangire nyumba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Hiramu mfumu ya ku Turo inatumiza amithenga kwa Davide pamodzi ndi mitengo ya mkungudza ndiponso amisiri a miyala ndi amisiri a matabwa kuti adzamumangire nyumba yaufumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Hiramu mfumu ya Turo anatumiza mithenga kwa Davide, ndi mikungudza, ndi amisiri omanga miyala, ndi amatabwa, kuti ammangire nyumba.