1 Chronicles 14:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Davide adafunsa kwa Mulungu kuti, “Kodi ndipite kukamenyana nawo nkhondo Afilistiwo? Kodi mudzaŵapereka m'manja mwanga?” Chauta adamuuza kuti, “Inde, pita. Ndidzaŵaperekadi m'manja mwako.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anafunsira kwa Mulungu, kuti, Ndikwere kodi kuyambana ndi Afilisti? Mudzawapereka m'dzanja langa kodi? Ndipo Yehova anati kwa iye, Kwera, pakuti ndidzawapereka m'dzanja lako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anafunsa Mulungu kuti, “Kodi ndipite kukathira nkhondo Afilisti? Kodi mukawapereka mʼmanja mwanga?” Yehova anamuyankha kuti, “Pita, Ine ndidzawapereka mʼmanja mwako.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anafunsira kwa Mulungu, kun, Ndikwere kodi kuyambana ndi Afilisti? mudzawapereka m'dzanja langa kodi? Ndipo Yehova anati kwa iye, Kwera, pakuti ndidzawapereka m'dzanja lako.