1 Chronicles 14:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Davide adapita ku Baala-Perazimu, ndipo adagonjetsa Afilistiwo kumeneko. Tsono adati, “Ndi dzanja langa Mulungu waŵang'amba pakati adani anga ngati madzi a chigumula.” Nchifukwa chake malo amenewo amatchedwa kuti Baala-Perazimu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atafika tsono ku Baala-Perazimu, Davide anawakantha komweko; nati Davide, Mulungu anapasula adani anga ndi dzanja langa, ngati pokhamulira madzi. Chifukwa chake analitcha dzina la malowo Baala-Perazimu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Davide ndi anthu ake anapita ku Baala-Perazimu ndi kugonjetsa Afilistiwo. Iye anati, “Monga amasefukira madzi, Mulungu waphwanya adani anga ine ndikuona.” Motero anawatcha malowa Baala Perazimu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atafika tsono ku Baala Perazimu, Davide anawakantha komweko; nati Davide, Mulungu anapasula adani anga ndi dzanja langa, ngati pokhamulira madzi. Cifukwa cace analicha dzina la malowo Baala Perazimu.