1 Chronicles 14:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Afilisti atamva kuti Davide wadzozedwa kukhala mfumu yolamulira dziko lonse la Aisraele, adapita onse kukamfunafuna. Davide atamva zimenezo, adatuluka kukamenyana nawo nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene Afilisti anamva kuti anamdzoza Davide akhale mfumu ya Aisraele onse, Afilisti onse anakwera kufunafuna Davide; ndipo Davide anamva, nawatulukira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Afilisti atamva kuti Davide wadzozedwa kukhala mfumu ya dziko lonse la Israeli, iwo anapita mwamphamvu kukamusakasaka. Koma Davide atamva zimenezi anapita kukakumana nawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene Afilisti anamva kuti anamdzoza Davide akhale mfumu ya Aisrayeli onse, Afilisti onse anakwera kufunafuna Davide; ndipo Davide anamva, nawaturukira.