1 Chronicles 15:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide adadzimangira nyumba zina mu mzinda wa Davide. Adakonza malo a Bokosi lachipangano la Chauta, namanga hema loikamo Bokosilo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anadzimangira nyumba m'mudzi mwake, nakonzeratu malo likasa la Mulungu, naliutsira hema.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide atadzimangira nyumba zina mu Mzinda wa Davide, iye anakonza malo a Bokosi la Mulungu ndipo analimangira tenti.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anadzimangira nyumba m'mudzi mwace, nakonzeratu malo likasa la Mulungu, naliutsira hema.