1 Chronicles 15:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Davide adalamulanso atsogoleri a Alevi kuti asankhe ena mwa abale ao, kuti aziimba ndi kuliza mwamphamvu zipangizo zoimbira monga azeze, apangwe, ndiponso ziwaya zamalipenga, kuti mau achimwemwe amveke bwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide ananena ndi mkulu wa Alevi kuti aike abale ao oimbawo ndi zoimbira, zisakasa, ndi azeze, ndi nsanje, azimveketse ndi kukweza mau ao ndi chimwemwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anawuza atsogoleri a Alevi kuti asankhe abale awo kuti akhale oyimba nyimbo zachisangalalo, zoyimba ndi zida: azeze, apangwe ndi ziwaya za malipenga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide ananena ndi mkuru wa Alevi kuti aike abale ao oyimbawo ndi zoyimbira, zisakasa, ndi azeze, ndi nsanje, azimveketse ndi kukweza mau ao ndi cimwemwe.