1 Chronicles 15:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Davide adati, “Alevi okha ndiwo amene asenze Bokosi lachipangano la Mulungu, wina aliyense ai, pakuti Chauta adasankhula Aleviwo kuti azisenza Bokosilo ndiponso kuti azimtumikira mpaka muyaya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Davide anati, Sayenera ena kusenza likasa la Mulungu koma Alevi ndiwo; pakuti Yehova anawasankha iwo kusenza likasa la Mulungu, ndi kumtumikira Iye kosatha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Davide anati, “Palibe wina ati anyamule Bokosi la Mulungu koma Alevi chifukwa Yehova anawasankha kuti azinyamula Bokosi la Yehova ndi kumatumikira pamaso pake nthawi zonse.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Davide anati, Sayenera ena kusenza likasa la Mulungu koma Alevi ndiwo; pakuti Yehova anawasankha iwo kusenza likasa la Mulungu, ndi kumtumikira iye kosatha.