1 Chronicles 15:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Davide pamodzi ndi akuluakulu a Aisraele ndiponso atsogoleri a ankhondo zikwi-zikwi, adapita mokondwera kuti akatenge Bokosi lachipangano la Chauta kunyumba kwa Obededomu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo Davide, ndi akuluakulu a Israele, ndi atsogoleri a zikwi, anamuka kukwera nalo likasa la chipangano la Yehova, kuchokera kunyumba ya Obededomu mokondwera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Davide pamodzi ndi akuluakulu a Israeli ndiponso asilikali olamulira magulu a anthu 1,000, anapita kukatenga Bokosi la Chipangano la Yehova ku nyumba ya Obedi-Edomu akukondwera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo Davide, ndi akuru akuru a Israyeli, ndi atsogoleri a zikwi, anamuka kukwera nalo likasa la cipangano la Yehova, kucokera ku nyumba ya Obedi Edomu mokondwera.