1 Chronicles 15:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide anali atavala mkanjo wabafuta wa thonje losalala, monga momwe adavalira Alevi amene ankanyamula Bokosi lachipangano, kudzanso anthu oimba ndiponso Kenaniya mtsogoleri wa anthu oimba nyimbo. Koma Davide adaavalanso efodi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anavala malaya abafuta, ndi Alevi onse akunyamula likasa, ndi oimba, ndi Kenaniya woyang'anira kusenzaku, pamodzi ndi oimba; Davide anavalanso efodi wabafuta.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Davide anali atavala mkanjo wa nsalu yofewa yosalala, monga anavalira Alevi onse amene ananyamula bokosi pamodzi anthu oyimba, ndiponso Kenaniya, amene anali woyangʼanira magulu oyimba. Davide anavalanso efodi ya nsalu yofewa yosalala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anabvala maraya abafuta, ndi Alevi onse akunyamula likasa, ndi oyimba, ndi Kenaniya woyang'anira kusenzaku, pamodzi ndi oyimba; Davide anabvalanso efodi wabafuta.