1 Chronicles 15:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Bokosi lachipangano lija lidadza ku mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo, adasuzumira pa windo, naona mfumu Davide akulumphalumpha ndi kuvina. Pamenepo mkaziyo adayamba kunyoza Davide mumtima mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo polowa likasa la chipangano la Yehova m'mudzi wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo anasuzumira pazenera, nao mfumu Davide alikutumphatumpha ndi kusewera; ndipo anampeputsa mumtima mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Bokosi la Chipangano la Yehova likulowa mu Mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Sauli ankaona ali pa zenera. Ndipo ataona Mfumu Davide ikuvina ndi kukondwera, iye ananyoza Davideyo mu mtima mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo polowa likasa la cipangano la Yehova m'mudzi wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Sauli anasuzumira pazenera, naona mfumu Davide alikutumphatumpha ndi kusewera; ndipo anampeputsa mumtima mwace.