1 Chronicles 16:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka adagaŵira Aisraele onsewo, amuna ndi akazi, aliyense mtanda wa buledi, nthuli ya nyama ndiponso keke ya mphesa zouma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nagwira aliyense wa Israele, wamwamuna ndi wamkazi, yense mtanda wa mkate, ndi nthuli ya nyama, ndi nchinchi ya mphesa zouma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka anagawira Mwisraeli aliyense, wamwamuna ndi wamkazi, aliyense buledi mmodzi, nthuli yanyama ndiponso keke yamphesa zowuma.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nagwira ali yense wa Israyeli, wamwamuna ndi wamkazi, yense mtanda wa mkate, ndi nthuli ya nyama, ndi ncinci ya mphesa zouma.