1 Chronicles 16:35 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munenenso kuti, “Tipulumutseni, Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, mutisonkhanitse ndi kutilanditsa kwa mitundu ina ya anthu, kuti tikuthokozeni potchula dzina lanu loyera, ndi kuti tizinyadira pokutamandani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nimunene, Tipulumutseni, Mulungu wa chipulumutso chathu; mutisokolotse ndi kutilanditsa kwa amitundu, kuti tiyamike dzina lanu loyera, ndi kudzitamandira nacho chilemekezo chanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Fuwulani kuti, “Tipulumutseni, Inu Mulungu wa chipulumutso chathu, mutisonkhanitse ndipo mutipulumutse kwa anthu a mitundu ina, kuti tiyamike dzina lanu loyera, kuti tikutamandeni.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nimunene, Tipulumutseni, Mulungu wa cipulumutso cathu; Mutisokolotse ndi kutilanditsa kwa amitundu, Kuti tiyamike dzina lanu loyera, Ndi kudzitamandira naco cilemekezo canu.