1 Chronicles 16:41 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthuwo anali pamodzi ndi Hemani ndi Yedutuni, kudzanso onse otsala amene adasankhidwa moŵatchula maina, kuti azithokoza Chauta, chifukwa cha chikondi chake chosasinthika ndi chamuyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi pamodzi nao Hemani, ndi Yedutuni, ndi osankhika otsalawo, otchulidwa maina, kuyamika Yehova; pakuti chifundo chake nchosatha;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthuwo anali pamodzi ndi Hemani ndi Yedutuni ndi onse amene anawasankha mowatchula dzina kuti apereke mayamiko kwa Yehova, “pakuti chikondi chake ndi chosatha.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi pamodzi nao Hemani, ndi Yedutuni, ndi osankhika otsalawo, ochulidwa maina, kuyamika Yehova; pakuti cifundo cace ncosatha;